Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:10 - Buku Lopatulika

10 Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Musachifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Musaŵauze zimenezi a ku Gati, musalire konse. Muvimvinizike m'fumbi ku Beteleafura, kuwonetsa chisoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Musanene zimenezi ku Gati; musalire nʼkomwe. Mugubuduzike mu fumbi ku Beti-Leafura.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:10
7 Mawu Ofanana  

Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.


Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'maphulusa.


Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.


Aike kamwa lake m'fumbi; kapena chilipo chiyembekezo.


Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.


Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.


ndi Avimu ndi Para, ndi Ofura;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa