Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:11 - Buku Lopatulika

11 Pitiratu, wokhala mu Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala mu Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala m'Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Inu anthu a ku Safiri mudzapita ku ukapolo muli maliseche ndi amanyazi. Anthu a ku Zanani satuluka mu mzinda wao. Mukamva anthu a ku Betezele akulira, mudzadziŵa kuti sangathe kukuthandizani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Inu anthu okhala ku Safiro, muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi. Iwo amene akukhala ku Zanaani sadzatuluka. Beti-Ezeli akulira mwachisoni; chitetezo chake chakuchokerani.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:11
12 Mawu Ofanana  

Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito.


Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zitendene zako zaphwetekwa.


Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m'chipululu.


Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; mizinda yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.


chifukwa chake taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwavundukulira umaliseche wako, kuti aone umaliseche wako wonse.


ndipo adzachita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira ntchito, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa; ndi umaliseche wa zigololo zako udzavulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.


Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.


Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako.


Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.


Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa