Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti wokhala mu Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti wokhala m'Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu a ku Maroti ali ndi nkhaŵa poyembekeza thandizo, chifukwa Chauta wadzetsa chiwonongeko pafupi ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu, akuyembekezera thandizo, chifukwa Yehova wabweretsa tsoka, lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:12
9 Mawu Ofanana  

Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa, ndipo polindira kuunika unadza mdima.


Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.


Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!


Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!


Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?


Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu.


Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.


Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa