Mika 1:13 - Buku Lopatulika13 Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala mu Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Mangani akavalo ku magaleta, inu anthu a ku Lakisi. Mudatsanzira machimo a Israele, potero mudachimwitsa anthu a ku Ziyoni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Inu anthu okhala ku Lakisi mangani akavalo ku magaleta. Inu amene munayamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti zolakwa za Israeli zinapezeka pakati panu. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.