Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Samariya, zilonda za uchimo wake sizingathe kupola, zafika mpaka ku Yuda. Chiwonongeko chili pafupi ndi mzinda wa anthu anga, chafika mpaka ku Yerusalemu kwenikweni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika; chafika ku Yuda. Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga, mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:9
15 Mawu Ofanana  

Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Koma panali chaka chakhumi ndi chinai cha mfumu Hezekiya, Senakeribu, mfumu ya Asiriya anadza, nathira nkhondo pa mizinda ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.


Ndipo mfumu ya Asiriya inatumiza kazembe kuchokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima chifupi ndi mcherenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu.


Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?


Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.


Pakuti wokhala mu Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.


Chifukwa chake Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula chifukwa cha zochimwa zako.


Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa