Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:8 - Buku Lopatulika

8 Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono Mika adati, “Nchifukwa chake ndidzalira komvetsa chisoni. Ndidzayenda maliseche, ndidzakuwa ngati nkhandwe ndi kulira ngati nthiŵatiŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni; ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche. Ndidzafuwula ngati nkhandwe ndi kulira ngati kadzidzi.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:8
19 Mawu Ofanana  

Chaka chakhumi ndi zinai cha Hezekiya Senakeribu mfumu ya Asiriya anakwerera mizinda yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.


Koma podziwa Mordekai zonse zidachitikazi, Mordekai anang'amba zovala zake, navala chiguduli ndi mapulusa, natuluka pakati pa mzinda, nafuula, nalira kulira kwakukulu ndi kowawa,


Ndili mbale wao wa ankhandwe, ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.


Ndikunga vuwo m'chipululu; ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.


Koma zilombo za m'chipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo.


Ndipo mimbulu idzalira m'maboma ao, ndi ankhandwe m'manyumba ao abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachuluka.


Chifukwa chake ndidzalira ndi kulira kwa Yazere, chifukwa cha mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleyale; chifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mfuu wankhondo wagwera.


Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.


Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.


Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Pakuti mau a kulira amveka mu Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.


Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Ejipito, nuwagwetsere iye ndi ana aakazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.


Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa