Ndidikira, ndikhala ngati mbalame ili yokha pamwamba pa tsindwi.
Ndimagona osapeza tulo, ndili ngati mbalame yokhala yokha pa denga,
Ndimagona osapeza tulo; ndakhala ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
Ndili mbale wao wa ankhandwe, ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.
Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.
Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete.
Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; ndipo anansi anga aima patali.
Mundikhalitsa maso; ndigwidwa mtima wosanena kanthu.