Masalimo 102:12 - Buku Lopatulika Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Inu Chauta, mumakhala pa mpando wanu waufumu mpaka muyaya. Anthu a mibadwo yonse adzakukumbukirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya; kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse. |
Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;
Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo.
Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.
Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.
Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.