Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 109:23 - Buku Lopatulika

23 Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:23
10 Mawu Ofanana  

Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.


Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.


Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.


Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.


Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.


Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?


koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.


inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa