Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 9:7 - Buku Lopatulika

Ndipo Herode chiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Herode chiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu Herode atamva zonse zimene zinkachitika zija, zidamuthetsa nzeru, chifukwa ena ankanena kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa,

Onani mutuwo



Luka 9:7
13 Mawu Ofanana  

Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Pakuti nditsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, lochokera kwa Ambuye, Yehova wa makamu, m'chigwa cha masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kufuulira kumapiri.


Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.


Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,


Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.


Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha Inu.


Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkokomo wake wa nyanja ndi mafunde ake;


Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa.


Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;


Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.