Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 21:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkokomo wake wa nyanja ndi mafunde ake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:25
26 Mawu Ofanana  

Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.


Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.


Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!


Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.


Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake.


Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ake akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lake.


Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.


Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.


Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.


Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:


Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.


Koma m'masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake,


Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero.


Ndipo pofika ora lachisanu ndi chimodzi, panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.


Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa