Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
Luka 3:2 - Buku Lopatulika pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo Anasi ndi Kayafa anali akulu a ansembe onse. Pa nthaŵi imeneyo Mulungu adampatsira uthenga Yohane uja, mwana wa Zakariya, m'chipululu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. |
Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.
anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.
Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.
Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.
Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?
Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;
Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.
ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Aleksandro, ndi onse amene anali a fuko la mkulu wa ansembe.