Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 1:2 - Buku Lopatulika

2 Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Udayamba monga mneneri Yesaya adalembera m'buku mwake kuti, “Mulungu akuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga m'tsogolo mwako kuti akakonzeretu njira yoti iwe udzapitemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya: “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu, amene adzakonza njira yanu,”

Onani mutuwo Koperani




Marko 1:2
13 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine,


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.


Ndipo anamuuza iye, Mu Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,


Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.


Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,


Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.


Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa