Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:1 - Buku Lopatulika

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa nthaŵi ya ufumu wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda, Chauta adampatsa mthenga Mika wa ku Moreseti. Nazi zimene iyeyu adaona m'masomphenya zokhudza Samariya ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:1
27 Mawu Ofanana  

Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.


Chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake,


Hezekiya analowa ufumu wake ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Abiya mwana wa Zekariya.


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.


Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana.


ndipo mutu wa Efuremu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa mizinda yamalinga; koma ndidzatumizira mizinda yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Tsoka osalabadirawo mu Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!


Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israele. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Si ndiyo Yerusalemu?


Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.


Katundu adamuona mneneri Habakuku


pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa