Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 1:2 - Buku Lopatulika

2 Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m'Kachisi wake wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Imvani nonsenu anthu a mitundu yonse. Tchera khutu iwe dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Ambuye Chauta akuimbani mlandu, akulankhulira ku Nyumba yao yoyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tamverani, inu anthu a mitundu yonse, mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo, pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani, Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Mika 1:2
33 Mawu Ofanana  

Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.


Nati Mikaya, Mukakabwera ndi mtendere konse, Yehova sananene mwa ine. Nati iye, Tamverani, anthu inu nonsenu.


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Ndikamva njala, sindidzakuuza, pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.


Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe, Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.


Ndinu ndikuitanani, amuna, mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.


Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.


Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika padziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.


Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.


Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova.


chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.


Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.


Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana.


Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.


Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Kumwamba kutchere khutu, ndipo ndidzanena; ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Ndipo akulu a Giliyadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kuchita monga momwe wanena.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa