Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 1:1 - Buku Lopatulika

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa nthaŵi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya ku Yuda, Chauta adamupatsa uthenga Zefaniya, mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 1:1
12 Mawu Ofanana  

Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m'munda wa nyumba yake, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwake Amoni mwana wake.


Naikidwa iye m'manda mwake m'munda wa Uza; nakhala mfumu m'malo mwake Yosiya mwana wake.


Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.


Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse;


Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvere.


anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:


Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa