ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Luka 1:53 - Buku Lopatulika Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu anjala waŵakhutitsa ndi zabwino, anthu olemera nkuŵabweza osaŵapatsa kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino koma anachotsa olemera wopanda kanthu. |
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.
Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka.
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;
Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.
Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.