Genesis 7:13 - Buku Lopatulika Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lomwelo, Nowa ndi mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi akazi ao, adaloŵa m'chombomo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo. |
Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.
Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.
iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa padziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu.
Mwezi wachiwiri tsiku la makumi awiri kudza asanu ndi awiri la mwezi, lidauma dziko lapansi.
Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;
ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;
Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkhe awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.