Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 2:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mulungu sadaŵalekererenso anthu akale aja, koma adangosunga Nowa yekha, mlaliki wa chilungamo, pamodzi ndi anzake asanu ndi aŵiri, pamene adadzetsa chigumula pa dziko la anthu osasamala za Iye Mulunguyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 2:5
12 Mawu Ofanana  

Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.


Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.


pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,


Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.


mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa