Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Genesis 5:32 - Buku Lopatulika Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nowa ali wa zaka zopitirira 500, adabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti. |
Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.
masiku ake onse a Lameki anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwalira.
Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao:
Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali padziko lapansi.