Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 10:32 - Buku Lopatulika

32 Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, chitapita chigumula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Onseŵa ndiwo mafuko a zidzukulu za Nowa potsata mibadwo yao ndi mitundu yao. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idatuluka mwa mafuko a Nowa ameneŵa, chitatha chigumula chija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 10:32
12 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.


Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.


Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.


Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.


Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.


Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.


Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.


Amenewa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.


Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane padziko lapansi, nimuchuluke m'menemo.


ndiwo amene analandira okha dzikoli, wosapita mlendo pakati pao.


ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa