Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 48:7 - Buku Lopatulika

Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndachita zimenezi chifukwa chakuti pamene ndinkabwerera kuchokera ku Mesopotamiya, mai wako Rakele adafera m'dziko la Kanani, mtunda wofika ku Efurata ukadalipo. Chisoni changa chinali chachikulu. Tsono ndidamuika komweko pa mseu wa ku Efurata ku Betelehemu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).

Onani mutuwo



Genesis 48:7
13 Mawu Ofanana  

ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.


Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pake: umenewo ndi choimiritsa cha pa manda a Rakele kufikira lero.


Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera mu Padanaramu, namdalitsa iye.


Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m'cholowa chao.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.


Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.


Ndipo panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Elikana, mwana wake wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, Mwefuremu.


M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezeka; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?


Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mzindawo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?


Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.