Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 2:18 - Buku Lopatulika

18 Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Mau anamveka m'Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 “Mau akumveka ku Rama, kulira ndi kubuma kwambiri: Rakele akulira ana ake. Akukana kumtonthoza, chifukwa ana ake asoŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Kulira kukumveka ku Rama, kubuma ndi kulira kwakukulu, Rakele akulirira ana ake; sakutonthozeka, chifukwa ana akewo palibe.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 2:18
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwera kwa abale ake, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti?


Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.


Koma munthu akufa atachita liondeonde inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?


Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.


Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,


Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.


Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa