Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 33:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Pambuyo pake Yakobe adakafika bwino ku mzinda wa Sekemu m'dziko la Kanani, atabwerera kuchokera ku Mesopotamiya. Adamanga mahema pamalo pena, poyang'anana ndi mzindawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mmene ankabwerera kuchokera ku Padanaramu, Yakobo anafika ku Salemu, mzinda wa Sekemu ku Kanaani. Anamanga msasa pamalopo moyangʼanana ndi mzindawo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:18
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako.


Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m'phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m'phiri la Giliyadi.


Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera mu Padanaramu, namdalitsa iye.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta mu Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.


Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.


Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera, ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.


anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.


Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.


Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;


ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.


Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzionetsa pamaso pa Mulungu.


Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa