Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 33:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma Yakobe adapita ku Sukoti, ndipo adamangako nyumba yake, pamodzi ndi makola a zoŵeta zake. Nchifukwa chake malowo adatchedwa Sukoti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Komabe Yakobo anapita ku Sukoti. Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Sukoti.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:17
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Esau anabwerera tsiku lomwelo kunka ku Seiri.


Mfumu inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zaretani.


Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera, ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.


Ndipo anachokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a chipululu.


ndipo m'chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum'mawa.


Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ake amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.


Ndipo anagwira akulu a m'mzinda ndi minga ya kuchipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.


Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani.


Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa