Rute 1:2 - Buku Lopatulika2 Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Munthuyo anali Elimeleki, mkazi wake anali Naomi. Ana ake aŵiriwo anali Maloni ndi Kiliyoni. Onsewo anali Aefurati a ku Betelehemu m'dziko la Yuda, koma adapita ku Mowabu nakhala komweko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Dzina la munthuyo linali Elimeleki, dzina la mkazi wake linali Naomi, ndipo mayina a ana awo aamuna anali Maaloni ndi Kiliyoni. Iwo anali Aefurati ochokera ku Betelehemu ku Yuda. Ndipo anapita kukakhala ku Mowabu. Onani mutuwo |