Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 35:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera mu Padanaramu, namdalitsa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera m'Padanaramu, namdalitsa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yakobe atabwerako ku Mesopotamiya kuja, Mulungu adamuwonekeranso namudalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yakobo atabwera kuchokera ku Padanaramu, Mulungu anabweranso kwa iye namudalitsa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 35:9
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Ejipito, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe;


Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;


Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.


Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye.


Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.


Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.


inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;


ndiye Yehova Mulungu wa makamu, chikumbukiro chake ndi Yehova.


Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa