Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.
Genesis 41:54 - Buku Lopatulika Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kudafika zaka zisanu ndi ziŵiri za njala zimene ankanena Yosefe zija. Njala imeneyo inali itafikanso ku maiko ena onse, koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya chambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo zaka zisanu ndi ziwiri za njala zija zinayamba monga ananenera Yosefe. Njalayi inafika ku mayiko ena onse koma ku dziko lonse la Igupto kunali chakudya. |
Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.
ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;
Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.
ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.
Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo.
Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.
Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani yense, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeze chakudya makolo athu.