2 Mafumu 8:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Ndiye kuti Elisa anali atauza mai amene adaamuukitsira mwana wake uja kuti, “Nyamuka upite pamodzi ndi a pabanja pako, ukakhale nawo kulikonse kumene ungathe kukakhala, pakuti Chauta akubweretsa pa dziko njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.” Onani mutuwo |
Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.