Genesis 41:27 - Buku Lopatulika27 Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zoonda zimene zidabwera pambuyo zija, ndiponso ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zopserera ndi mphepo yakuvuma zija, ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndi zosaoneka bwino zimene zinatuluka pambuyozo ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zachabechabe, zowauka ndi mphepo ya kummawa zija ndi zaka zisanu ndi ziwiri za njala. Onani mutuwo |