Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:30 - Buku Lopatulika

30 ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Zitapita zaka zimenezo, padzakhalanso zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, ndipo zaka zonse zija za dzinthu zidzaiŵalika mu Ejipito monse. Njalayo idzaononga dziko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 koma zidzatsatana ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njala. Chakudya chochuluka cha mu Igupto chija chidzayiwalika ndipo njalayo idzawononga dziko.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:30
15 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene zinadya sizinadziwike kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba.


Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.


ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzavuta.


Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.


Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya.


Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.


Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo.


Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.


Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.


Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate.


amwe, naiwale umphawi wake, osakumbukiranso vuto lake.


chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.


Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;


Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa