Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani tinalefuka chifukwa cha njalayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Njala ija idakula kwambiri, kotero kuti panalibe chakudya pa dziko lonse lapansi, ndipo anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani komwe adafooka nayo njalayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Njala inakula kwambiri motero kuti chakudya chinasowa mʼdziko lonse. Anthu a ku Igupto ndi ku Kanaani analefuka nayo njalayo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:13
9 Mawu Ofanana  

Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.


Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.


Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupserera monga chipululu, kuti anthu asapitemo?


Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.


Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani yense, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeze chakudya makolo athu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa