Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Yosefe adasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a ku Ejipito pamodzi ndi a ku Kanani adaamwaza pogula tirigu. Ndalama zonsezo adazitenga napita nazo kunyumba kwa Farao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a mu Igupto ndi Kanaani ankapereka pogula tirigu, ndipo anabwera nazo ku nyumba kwa Farao.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:14
8 Mawu Ofanana  

Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.


Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.


Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama.


Womana tirigu anthu amtemberera; koma madalitso adzakhala pamutu pa wogulitsa.


Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.


monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa