Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yosefe adapereka chakudya kwa bambo wake ndi kwa abale ake ndi kwa mbumba yonse, potsata kuchuluka kwa ana ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Yosefe anaperekanso chakudya kwa abambo ake, kwa abale ake ndi kwa onse a mʼnyumba ya abambo ake monga mwa chiwerengero cha ana awo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:12
16 Mawu Ofanana  

Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;


ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.


Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikulu.


Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anachokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni.


Tsono anthu, anasunthira iwo kumizinda kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake.


Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.


Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu aang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.


Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.


Ndipo iwo adzapachika pa iye ulemerero wonse wa banja la atate wake, obadwa ndi ana, mbiya zonse zazing'ono, ngakhale zikho ndi aguda omwe.


Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ake a iye yekha;


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.


Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.


Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana aamuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa