Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti m'Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndikumva kuti ku Ejipito aliko tirigu. Pitaniko kumeneko, mukatigulireko ife, kuti tingafe ndi njala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ine ndamva kuti ku Igupto kuli tirigu. Pitani kumeneko mukatigulireko kuti tisafe ndi njala.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu mu Ejipito.


Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono.


Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya.


Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.


Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe.


Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.


Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.


Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.


Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu mu Ejipito, anatuma makolo athu ulendo woyamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa