Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 4:6 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi wakwiyiranji chotere? Chifukwa chiyani nkhope yako yagwa?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa?

Onani mutuwo



Genesis 4:6
13 Mawu Ofanana  

Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.


Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.


Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?


atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?


Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?


Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.


Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?