Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 4:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi wachita bwino pokwiya chifukwa cha msatsiwu?” Iye adati, “Inde ndachita bwino kukwiya. Kukwiya kwake nkofa nako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma Mulungu anati kwa Yona, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye chifukwa cha msatsi?” Iye anayankha kuti, “Inde nʼkoyenera. Kukwiya kwanga nʼkofuna kufa nako.”

Onani mutuwo Koperani




Yona 4:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.


Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako, kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe? Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwake?


Pakuti muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo; ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.


Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Koma sikudakomere Yona konse, ndipo anapsa mtima.


Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirepo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;


Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.


Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.


Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ake, namkakamiza, moyo wake unavutika nkufuna kufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa