Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 4:5 - Buku Lopatulika

5 koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, ndipo nkhope yake inagwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma Kaini Chauta sadakondwere naye ndipo sadalandire chopereka chake. Chifukwa cha zimenezi, Kainiyo adakwiya kwambiri, kotero kuti nkhope yake inali yakugwa ndi yamasinya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 4:5
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekere iye monga kale.


ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.


Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima.


Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako.


Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza;


Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.


Anthu ankhanza ada wangwiro; koma oongoka mtima asamalira moyo wake.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.


Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.


Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa