Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
Genesis 38:12 - Buku Lopatulika Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita nthaŵi, mkazi wa Yuda uja, mwana wa Suwa, adamwalira. Tsono Yuda atatha kulira malirowo, iyeyo pamodzi ndi bwenzi lake Hira Mwadulamu, adapita ku Timna kumene ankameta nkhosa zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo. |
Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.
Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, chifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Aminoni.
Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna;
Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.