Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Genesis 33:3 - Buku Lopatulika Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe adatsogola, ndipo adaŵerama mpaka pansi kasanu ndi kaŵiri akuyandikira mbale wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye mwini anakhala patsogolo nawerama mpaka kukhudza pansi kasanu ndi kawiri pamene amayandikira mʼbale wake. |
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse.
Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.
Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.
Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse; popeza walowa m'dzanja la mnzako, pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako.
Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.