Genesis 42:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono popeza kuti Yosefe anali nduna yaikulu yolamulira dziko lonse la Ejipito, ndiye amene ankagulitsa tirigu kwa anthu ochokera ku mbali zonse za dziko. Choncho abale ake a Yosefe nawonso adabwera, ndipo adamgwadira Yosefeyo, namuŵeramira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Pakuti Yosefe anali nduna yayikulu yolamulira dziko la Igupto, ndiye kuti analinso amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse. Choncho abale ake a Yosefe nawonso anabwera, ndipo anamugwadira pansi. Onani mutuwo |