Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye.
Genesis 32:2 - Buku Lopatulika Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ataŵaona, adati, “Ili ndi gulu la ankhondo a Mulungu.” Motero malowo adaŵatcha Mahanaimu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Yakobo anawaona anati, “Ili ndi gulu la Mulungu.” Choncho anawatcha malowo Mahanaimu. |
Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye.
Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga.
Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.
Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikulu, ngati nkhondo ya Mulungu.
Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe; bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe. Muyang'aniranji pa Msulami, ngati pa masewero akuguba?
Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki.
Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,
Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;
Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?