1 Mafumu 2:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 “Palinso Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, amene adaanditukwana momvetsa chisoni, tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu. Koma pamene adadza kudzakumana nane ku Yordani, ndidalumbira m'dzina la Chauta kuti sindidzamupha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 “Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’ Onani mutuwo |