Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.
Genesis 27:12 - Buku Lopatulika Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwina mwake bambo wanga adzandikhudza, ndipo adzadziŵa kuti ndikumunyenga. Motero m'malo mondidalitsa, adzanditemberera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.” |
Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.
Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso?
mpaka utamchokera mkwiyo mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?
Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.
Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.
mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;