Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:10 - Buku Lopatulika

10 Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Ndi wotembereredwa amene amagwira ntchito ya Chauta mwaulesi. Ndi wotembereredwa amene amaletsa lupanga lake kutema ndi kupha anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika! Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:10
15 Mawu Ofanana  

Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva,


Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.


Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ake.


Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.


ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisraele: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili,


Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m'chimake; puma, nukhale chete.


Udzakhala chete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? Za Asikeloni, ndi za m'mphepete mwa nyanja, pamenepo analiika.


Yehova watsegula pa nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi ntchito m'dziko la Ababiloni.


Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.


koma inu musaime, pirikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'mizinda mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.


Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova, mutemberere chitemberere nzika zake; pakuti sanadzathandize Yehova, kumthandiza Yehova pa achamuna.


Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.


Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafune kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa