Genesis 23:3 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adasiya mtembo wa mkazi wakewo, nakalankhula ndi anthu a ku Hiti kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Abrahamu ananyamuka pamene panali mtembo wa mkazi wakepo kupita kukayankhula ndi anthu a ku Hiti. Ndipo anati, |
munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
m'phanga lili m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake:
Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.