Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli a siliva mazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu.
Genesis 23:16 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adavomera, ndipo pamaso pa anthu onse a ku Hiti adaŵerenga masekeli a siliva okwana 400 amene Efuroni adaatchula, potsata ndalama zomwe anthu amalonda ankagwiritsa ntchito m'dzikomo pa nthaŵi imeneyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito. |
Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli a siliva mazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu.
ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.
Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanitsidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti,
chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.
Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pamutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.
Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva.
Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.
Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.
Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.
Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu.
Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.
Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.