Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:21 - Buku Lopatulika

21 ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Titafika pa malo a chigono, pomasula matumba athu, aliyense mwa ife adapeza ndalama zake kukamwa kwa thumba lake, ndipo ndalamazo zinalipo zonse monga momwe tidaaŵerengera. Ndalama zimenezo tabwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 koma titafika pa malo ena kuti tigone, tinatsekula matumba athu ndipo aliyense wa ife anapeza ndalama zake momwe zinalili zili pakamwa pa thumba lake. Ndiye tabwerera nazo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:21
12 Mawu Ofanana  

nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;


Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe.


Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya:


Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu.


Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kutuluka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golide?


Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.


Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.


Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa