Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:16 - Buku Lopatulika

16 ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori m'Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pambuyo pake iye adaŵanyamula kupita nawo ku Sekemu, kumene adaŵaika m'manda amene Abrahamu adaagula ndi ndalama kwa ana a Hamori ku Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:16
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.


Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.


Ndipo anafa Rakele, naikidwa panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.


Ndipo ana ake aamuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo;


chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.


Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israele ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawasiya kuno.


Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa