2 Samueli 24:24 - Buku Lopatulika24 Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Koma mfumu idauza Arauna kuti, “Iyai, koma ndichita chogula ndithu kwa iwe pa mtengo wake. Sindingapereke ngati nsembe zopsereza kwa Chauta Mulungu wanga zinthu zosagula.” Choncho Davide adagula malo opunthirapo tirigu aja pamodzi ndi ng'ombe zomwe pa mtengo wa masekeli asiliva makumi asanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.” Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu. Onani mutuwo |